BUKU LANGA LA ALIFABETI
IMPACT NETWORK Samuel M Phiri

Amai ambeleka mwana.

1

Onani Buluzi akuyenda.

2

Agogo akusunga Cona wakuda.

3

Atsibweni agula Delesi la mwana.

4

Timaika kalata mu Emvelupu ikalembedwa.

5

Fulu ali ndi cigoba colimba kwambiri.

6

Onani Galimoto ikubwera.

7

Cheni yabwino iyenera kukhala ndi Huku.

8

Culu canga cimatuluka Inswa zaka zonse.

9

Agogo anga akonda kubvala Jaketi popita kuchalichi.

10

Kalulu ndi nyama yocenjela kwambiri panyama zamthengo zonse.

11

Muyoma akonda kudya lalanje.

12

Munthu afunika kukhala Ndi mpando panyumba kuti alendi azikhalapo akafika.

13

Nadzikambe ndi nyama yamthengo yomwe imasintha mitunthu Poziteteza ki adani.

14

Amalume agulitsa Ovolosi loyela.

15

Amai a Phika sima m'poto.

16

Atate agulitsa cikunje ca Repu wokongola komanso wobiliwira.

17

Sukulu la Kafunde ndi yaukhondo kwambiri.

18

Tomato ndi wabwino cifukwa umakometsa ndiwo.

19

Udzudzu umapasa anthu matenda ya malungo ngati sagona mukonde.

20

Muyama analiza vuvuzera kum'pira wamiyendo.

21

Wailesi ndiyabwino panyumba cifukwa imatiuza makhalidwe momwe tinga pewele matenda a kolona vairasi (covid-19).

22

Yesu analila. YOHANE 11:35

23

Munthu aliyense ayenera kukhala ndi zobvala kuti azioneka bwino.

24
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
BUKU LANGA LA ALIFABETI
Author - IMPACT NETWORK Samuel M Phiri
Illustration -
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs