Miyambo ya maliro ya ansenga
Zumani Mumba

Anthu akakhala pamodzi amathandizana zinthu zosiyana-siyana zimakhala zithu monga kubwerekana njinga, ngolo ndi zina zotere. Koma ngakhale ndi conco, mabvuto amakhalaponso monga imfa.
Imfa ndi bvuto lokhalo limapangitsa anthu ambiri

1

Ammudzi kusowa mtendere. Anthu amisinkhu yosiyana-siyana amamwalira ndipo, ndipo izi zikacitika, anthu ammudzi amakhudzidwa mosiyana. Ziri conco cifukwa pena kuma kumakhala kukhudzidwa cabe cifukwa amudziwa muthu omwalirayo, pomwe ena

2

Ncigukwa cakuti omwalirayo ndi wa cibale. Koma ngakhale ziri tero anthu mudzi wonse amakhala acisoni.
Pokhala imfa ndi bvuto lalikulu, panaikidwa miyambo yake yomwe iyenera kutsatiridwa. Mwambo woyamba kumakhala kuoka zitsamba mnjira

3

Posonyeza kuti mmudzi muli maliro. Ndipo anthu onse oyenda mnjira ayenera kusonyeza ulemu monga kutsika njinga ngati afika pamalopo. Ndipo anthu oika zitsamba ochedwa anungwe amamulipiritsa munthu ngati waswa lamulo limeneri.

4

Kunyumba nakonso kulimwambo wakuti, azimai onse amakhala pafupi ndi nyumba ya maliro pomwe ena amakhala mkati pafupi ndi anyamalira. Azibambo naonso amakhala ndi malo awo koma pafupi ndi nyumba ya maliro. Azimai kapena azibambo sabvomerezeka

5

Kukhala pa mipando. Ngati pali wasemphana ndi zimenezi amapatsidwa mlandu ndi kulipira ndalama ya ndapusa. Kubvala cisote nakonso kuletsedwa. Azibambo ndiwo amapanga bokosi kuti mtembo ugonemo. Anthu opanga bokosi amacita kusankha ndipo alipiridwa

6

Azibambo kubanja lofedwa amagula nsalu ya mtembo. Ndipo ikafika nthawi anungwe amauza anthu kukhala pamodzi kuti ayambe kayendrtsedwe ka maliro. Ndipo bokosi likanyamulidwa anyamalira amalira kwambiri. Mankhoswe amaonetsetsa kuti pali sopo

7

Wosambira kumanja. Ndipo izi zikatha, anungwe amakamba za mbiri ya omwalirayo, iwo amafotokoza zaka, dzina ndi banja imene wasiya kubwalo kuno kuthauza ana ake. Komanso matenda abweretsa imfa .

8

Ndipo mmodzi mwa anungwe amatumizidwa kumanda kukaona ngati anthu atsiriza kukumba manda. Ngati yankho ndi inde, ulendo wa kumanda uyambika koma ngati ndi ai, apo amayembekeza mpaka manda athe kukumba.

9

Pofika maliro kumanda, anthu onse amakhala oyimirira kusonyeza cisoni. Mtembo ukafika mdzenje anthu onse amakhala pansi ndipo anyamalira amapemphedwa kukhala cete. Ndipo anungwe amafotokoza cimodzi-modzi mbiri ya omwalira.

10

Ndipo amayamba kufocera dzenje, anyamalira pamenepo amayamba kuliranso. Zikatha izi amabwereranso kumudzi. Anthu onse akafika kumudzi amapatsidwa cakudya maka maka anthu ocokera kutali.

11

Azimai ammudzi amagona kunyumba ya maliro mpaka masiku awiri. Azimai amatsira nyumba munali mtembo ndipo akatero amacoka ndi kukhala ndi kugona kumanyumba kwawo apo mwambo wa maliro watha.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Miyambo ya maliro ya ansenga
Author - Zumani Mumba
Illustration -
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs