Kusowa kwa mwana wa a Mfumu
Impact Network and Moses Phiri

Kale-kale pamudzi wa a Cimangeni panali Mfumu dzina lake Tiyeseko. Mfumuyi inali ndi ana atatu; Ziyelesa, Samalani ndi Yamikani.
Anawa anali ndi maluso osiyana-siyana monga kulima mbeu za kumunda ndi zakudimba.

1

Munda wa a Mfumu Tiyeseko unali kufupi ndi dziwe lalikulu la madzi pamene panali nyama zosiyana-siyana kuphatikizapo mvuu.
Tsiku lina, Mfumu Tiyeseko anapita kumunda ndi ana ake.

2

Ziyelesa anakhalira kumbuyo. Iye anali kuwetera. Mwadzidzidzi, Ziyelesa anagwiridwa ndi mvuu ndikulowa naye pamadzi.

3

M'madzulo, a Mfumu anayetsetsa kufuna-funa mwana wake koma sanam'peze. Motero, Mfumu inaitana anthu onse pam'dzi ndi kuwadziwitsa zimene zawagwera. Anthu nawonso anayetsa njira zosiyana-siyana kusakila mwana wa Mfumu koma analephera.

4

Mfumu Tiyeseko anapita kum'dzi wina woyandikana nawo kumene kunali Sing'anga wina wotchuka kwambiri. Sing'angayu anauza Mfumu Tiyeseko zonse kuti mwana wao anagwiridwa ndi mvuu pamene anali kupita kumunda ndipo mvuu inalowa naye pamadzi.

5

Ndi kumukhomera mnyumba yace yapa madzi ndipo imayika fungulo mkamwa mwace.
Sin'ganga inapitiliza ndipo inati, pafunika anthu asanu; cawinda, woyendetsa bwato, wannabes, wotenga mfungulo ndi iye sin'ganga.

6

M'mawa kutaca, anthu asanu aja ananyamuka ndi kupita kumadzi. Woyendetsa bwato nayenso anagwira nchito yake kuwafitsa anthu aja komwe sin'ganga anakamba.

7

Atafika pamadzi, wanthabwala anayamba kucita nthabwala zake ndipo mvuu anaseka kucita kugwetsa misozi. Wotenga fungulu nayenso anagwira nchito yake ndikutsegula kunyumba ndipo anatenga mwana uja ndikulowa naye m'bwato apo mvuu ili kuseka.

8

Mvuu itatha kuseka inawona kuti anthu aja palibe pamodzi ndi mnyamata uja Ziyelesa. Pamenepo, mvuu inayamba ulondola. Ciwinda poona kuti mvuu ikubwera, anatenga mpaliro wake ndi kulasa mvuu. Mvuu ija inafelatu pamenepo.

9

Anthu aja anapitiliza ndi ulendo wawo m'paka anafika kumudzi ndi mwana uja. Mfumu Tiyeseko anaitana anthu ake kuzacita phwando. Kunali kudya, kumwa ndi kubvina tsiku limeneli.

10
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kusowa kwa mwana wa a Mfumu
Author - Impact Network and Moses Phiri
Illustration -
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs