

Kale-kale kunali atsikana awiri omwe amakondana kwambiri. Maina ao anali Malita ndi Maria. Atsikanawa anakulira pamodzi. Malita anali mtsikana opanda ulemu. Zaka zitapitapo, atsikanawa anapeza mabanja koma mwatsoka sanali kubereka.
Tsiku lina, atsikanawa anaganiza zopita ukafuna thandizo la mankhwala kwa sing'anga wina ochedwa Chekulako. Atafika kwa sin'ganga, Chekulako anawauza kuti akapange ulendo wa matsiku atatu.
Kutaca m'mawa, Malita ndi Maria anauyamba ulendo monga anawauzira sing'anga. M'madzulo dzuwa italowa, iwo anafika pamudzi wina pomwe anapempha Malo kuti agone. Atafika panyumba ina, iwo anapeza kuti pali nkhalamba yochedwa Cakumanda.
Gogo Cakumanda anawalandira atsikanawa ndipo anawauza kuti aphike nsima komanso ndiwo za mphusi zocokera pa zilonda za pathupi lace.
Malita kukhala mwana opanda ulemu anakana nati, "ucitsilu wanu, ndani azaphika nsima ndi kudya ndiwo za mphusi.
Mulibe nzeru inu." Koma Maria anacita momwe anawauzira agogo. Atasiliza kuphika, Malita anakana kudya ndipo anapita ukagona.
Maria anasamba kumanja monga azadya koma iye anali kuponya nsima kumbuyo kwake.
Atapitiliza kudya, gogo Cakumanda anati, "ndidziwa kuti mukufuna ana. Zomwe ndikuuzeni ndizakuti, paulendo uyu, uzapeza zinthu zosiyana-siyana. Uzapeza njoka zili kubvina, mitengo ili kugwa yokha ndiponso acule ali kuimba koma osaseka.
Kumapeto kwazonsezi uzapeza ng'oma zitatu. Ng'oma yoyamba izilira mba-mba-mba, yaciwiri izilira mbe-mbe-mbe ndipo yacitatu izilira ndu-ndu-ndu. Iwe ukasegule ng'oma yacitatu. Maria anati, "zikomo agogo."
Kutaca m'mawa, atsikana anauyamba ulendo wautali. Iwo anakumana ndi njoka zili kubvina ndipo Malita anaseka, "kkkkkkk, onani njoka zili kubvina." Patsogolo anapezanso acule ali kuimba. Malita anacita cimodzi-modzi.
Kothera kwazonse, Malita ndi Maria anapeza ng'oma zitatu. Maria anakumbukira mau a gogo Cakumanda ataona ng'oma. Iye anauza Malita zomwe agogo anamuuza koma Malita anatsutsa nati, "ndibodza imeneyo. Tele iwe ungakhulupilire nkhalamba ija.
ine ndizacita zomwe ndifuna.
Samva za anzake, anaviika nsima m'madzi. Malita uja anapita pa ng'oma zija ndipo anatsegula pa ng'oma yoyamba. Iye anapezapo mwana olemala. Mwanayu anali ndi dzanja limodzi, mwando umodzi, dzitu imodzi, mphuno yong'ambika pakati.
Zonse za mwanayu zinali cimodzi-cimodzi.
Maria anacita zomwe agogo Cakumanda anamuuza. Iye anatsegula ng'oma yacitatu ndipo anapezamo mwana okongola kwambiri. Malita
poona tero, anaonetsa kukwiya kwambiri ndipo atsikana anabwelera kum'dzi. Atafika kum'dzi, anthu anayamba kumseka Malita. Tsiku lina, Malita anauza Maria kuti apite kumtsinje kukachapa zobvala. Atafika kumtsinje, iwo anayamba kuchapa.
Maria anauza Malita kuti, "ndifuna kupita kuchire, undipenyeleko mwana." Malita anati, "Cabwino." Koma mumtima mwake anati, "uyu ndiwo mpata wanga." Iye anatenga mwana uja nati, anthu akundiseka kuti ndili ndi mwana olemala komanso oipa.
Koma tsopano, tizaona omwe adzatsekedwa. Iye anatenga mwana uja nam'ponya pamadzi. Atacita izi, Malita anathawa napita kumudzi.
Maria atafika kucokera kuchire anapeza kuti Malita palibe pomwe anali ndipo anayamba kumuitana mokwedza mau. Iye anati, "mwina Malita wapita kumudzi." Motero, Maria anaganiza kuti apite kumudzi. Atafika kumudzi, Maria anafunsa Malita komwe
mwana wace ali koma Malita anati, "sindidziwa komwe kuli mwana wako cifukwa ndamusiya kumtsinje. Atsikana aja anayamba kupanga phokoso m'mudzi ndipo anthu onse anabwera. Maria anapeleka nkhani kwa amfumu. Atsikana awiri aja anaitanidwa
kwa Mfumu. A Mfumu anafunsa Maria kuti afotokoze momwe zinaliri. Maria anafotokoza ndipo Malita anacita cimodzi-modzi. A Mfumu anaweludza kuti Maria atenge mwana wa Malita kuti nayenso akam'ponye pamadzi kuti onse akhale opanda mwana.
Maria anacita monga ananenera a Mfumu. Kucokera pamenepo, ubwenzi wa Maria ndi Malita unatha. Iwo sanagwirizaneponso pa umoyo wao.

