

Mayo, msana wanga ine! Analira finye atamunyamula m'mwamba ndi kumpanditsa kumwala. Inali ndeo yowopsa komanso ya fumbi.
Fulu lina, finye anali khale pacitsime pamene panali madzi ambiri ndiponso azidzira bwino. Finye sanali kufuna kuti
nyama zina zizikhala m'madzimo komanso kumwako madzi.
Nyama zosiyana-siyana zinali kubwera kuti zimweko madzi koma finye ankakalipa nazipilikitsa nyamazo. Nyama monga: afisi, akalulu, acule, njobvu ndi nyama zina zambiri zinali kubwera.
Finye amati akakalipa, amatumpha ndi kunyoza nyama zinzake. Akatero, iye anali kucotsa poizoni yoipa kwambiri yoyera ngati Mkaka. Nyama zina monga nyalubwe zinali kunena finye nati, "tizakumwela mkaka wako onse ndipo udzafa."
Nyalubwe pakufuna kupha finye anamwa mkaka uja cotsadziwa kuti ndi poizoni ndipo anafa.
Nyama zambiri zitaona zimenezi zinaopa kwambiri. "Haha! taonani nyalubwe waphedwa ndi kanyama kakang'ono kaja. Ine ndituluka m'madzi muno." Anatero
ng'ona kuuza nyama zinzake za m'madzi monga cule ndi nsomba.
Tsiku lina, nyama zosiyana-siyana zinakhala ndi mtsonkhano zitaona kuti zikhala ndi ludzu cifukwa ca finye. Zinafuna kuti zipeze njira yogonjetseramo finye. Njuci inati, ine ndine
ndingaphe finye. Ndizangomuluma pakamwa ndipo adzafa. Nyama zambiri zinazipeleka kuti zikaphe finye. "Yai, ndipita ndine." inatero njoka. ine ndiri ndimano opotsa iwe njuci komanso ulibe thupi monga ine. Iwe ndiwe wocepa.
Pothera pake, nyama zija zinagwirizana kuti njuci apite ukapha finye kuposa njoka cifukwa njuci ili ndi mapiko ndipo itha kuuluka.
Njuci inapita koma itafika, inapeza finye ali pamtunda kulonda madziwo. Lero ndikupha finye cifukwa
utiletsa kumwako madzi." Anatero njuci. Finye ankakalipa ndipo anauza njuci kuti, "ndikupha monga ndinaphera nyalubwe." Finye anatumpha nacotsa poizoni kenaka inakwera pamsana and pa finye namuluma pakamwa. Poizoni ija inalowa m'maso ndi
mkamwa mwa njuci ndipo posapita nthawi, njuci anamwalira.
Nyama zija zinali ciKhalid kuyembekedza njuci. "Kodi ndiye kuti waphedwa njuci monga nyalubwe?" anafunsa kalulu. Tiyeni tisankhe nyama yanzeru komanso yamphamvu ipite ukaona.
Njobvu inati, "tiyeni tonse pamodzi ndipo finye tizamupha pakumponda-ponda ndi kum'menya." Inde, iyi ndiye njira yokhayo cifukwa finye sangathe kupha tonse panthawi imodzi anatero ng'ona.
Koma mkango anati, tisapite pamodzi cifukwa finye
akaona gulu ya ife, adzathawa. Mobvomekedza, kalulu anati, inde, tisapite tonse cifukwa finye akadzaona gulu lathu adzathawa. Tumani ine ndipite. Monse mudziwa bwino kuti ndine nyama yocenjera kwambiri kuposa nyama zonse. Ndizamupha finye
mosavutika. ndapanga ganizo. Nditenga gitala kuti ndikamuyimbire finye. Iye akadzabvera mayimbidwe anga adzasangalala kwambiri. Telo ine ndidzamuomba ndi gitala m'mutu pamene iye akubvina.
Pakumva tero, nyama zija zinamva bwino ndipo
zinasangalala kwambiri ndipo zinati kuuza kalulu, ndiwedi nyama yocenjera kuposa tonsefe. Udzakwanilitsadi kupha finye kopanda cobvuta ciliconse.
Nyamazo zinayimba nyimbo mosangalala kutamanda kalulu. Zinayimba ng'ona, zipoliro, magitala
ndi kubvina kwambiri. Kalulu anamva bwino ataona nyama zinzake ziri kutamanda. Atasangalala tero, kalulu anauyamba ulendo opita ukapha finye. Panthawi imodzi-modzi, finye anali kuzipukuta poizoni omwe anaphela njuci. Iye ankati ngati
wapukuta poizoni uja, anali kuika pa dzani imene anathodola kumtengo m'mphepete mwa citsime ca madzi cija.
Iye anali kucotsa poizoni ouma pathupi lake anamva mau akuti, "bwenzi langa, kodi uliko?" Ao anali mau ocokera kwa kalulu.
Kalulu anafika pafupi napatsana moni moni ndi finye. Pambuyo pake, Kalulu anati kwa finye, tamvelako nyimbo mayimbidwe anga osangalatsa. Kalulu anayamba kuimba nyimbo ndi gitala yake. Yanali maimbidwe abwino komanso otenga mtima. Finye
anamva bwino nasangalala kwambiri ndipo anabvina onse pamodzi ndi kalulu. Kalulu ankabvinitsa kwambiri ciuno cake kenaka finye anali kubvina mopalasuka ndi miyendo ake.
Yanalidi mabvinidwe otenga anyama ziwiri zija. Mbalame, agulugufe,
nchenche ndi tunyama twina twa mumlenga-lenga tunadabwa ndi kucita cidwi ndi mabvinidwe akalulu ndi finye.
Ali cibvinire tero, kalulu anaona dzani ija pomwe panali Mkaka ouma wa poizoni naganiza kuti cinali cakudya cotsekemera.
Iye anaganiza kuti unali uci. Kalulu anatenga Mkaka wa poizoni uja ndi kudya cotsadziwitsa kapena kufunsa finye.
Kalulu anapitiliza kuimba nyimbo ndi gitala yake. Mwazizizi ali kuimba ndi kubvina, finye anaona Kalulu wagwa pansi nayamba
kukomoka ndipo pamalo panakhala ziiii. Finye anadabwa kwambiri cifukwa sanadziwe cimene cinapha kalulu.
Finye anakhala ndi cisoni cacikulu pa zomwe zinacitika. Poona kuti kwada, finye anatenga gitala ya kalulu nalowa nayo kumphako kumene
iye anali kugona imene inali mkati mwa citsime camadzi cija.
Nyama zija zomwe zinatuma Kalulu zinadabwa kuti kwada ndipo kalulu sanabwerere. Nyamazi zinazindikira kuti kalulu waphedwa ndi finye. Nyamazi zinazadzidwa ndi ukali kwambiri.
Tsiku lina, nyamazi zinatuma fulu kuti akagwire finye ndipo nyama zina zikakhale pafupi kuti zikathandizire.
Fulu anaikidwa ulimbo pamsana pake kuti finye adzagwiridwe ndi ulimbo. Iyi inalidi ganizo labwino kwambiri. Fulu anafika pafupi
ndi finye nakhala cete. Cotsadziwa, finye anabwera nakhala pamsana wa fulu. Iye anaganiza kuti wakhala pa mwala.
Thamangani! tabwelani mudzandiithandidze.! ndamugwira! ndamugwira! anakuwa fulu kuitana anzake aja.
Mayo! mayo ine! analira
finye atagwiridwa ndi nyama zinzake zija zimene anali kuletsa madzi.
Panalidi ndeo yaikulu kwambiri. kumvekere, thiii...! namupanda m'mutu. Finye sanafune kugonja ai. Njobvu inafuna kuponda finye pamsana koma finye analothoka nalowa
m'mphuno mwa njobvu ija ndipo inafa.

