Nthano ya Kalulu ndi fulu
Alifeyo Mkandawire and Impact Network

Kale-kale, panali nyama ziwiri zomwe zinali kunkhala m'mudzi umodzi. Maina a nyama zimenezi yanali Kalulu ndi fulu. Tsiku lina, panabuka mkangano pakati pa nyama ziwirizi.
Kalulu anati, "ine ndimathamanga kuposa nyama zonse." Fulu nayenso

1

anati, "ngakhale kuti umathamanga kwambiri, ndikhodza kufika mwamsanga kuposa iwe.
Pothesa mkangano umenewu, iwo anagwirizana kuti akacite mpikisano.

2

Tsiku lampikisano itafika, Kalulu ndi fulu anakumana kumalo ocitira mpikisano. Cule anafika kumalo kumeneko kuti akayambitse mpikisano. Mosataya nthawi, Cule anaimba wezulo kuyambitsa mpikisano.

3

Pomwe cule anaimba wezulo, Kalulu anaiyamba liwiro lafumbi ndipo sanayangane kumbuyo.
Ngakhale kuti Fulu analibe liwiro, iye anali naco ciyembekezo cacikulu cokhodza kupambana.
Pang'ono pang'ono, Fulu analondola m'mbuyo mwa Kalulu.

4

Kalulu poona kuti Fulu wakhalira, iye anaganiza nati, " ndamutsiya kutali kwambiri Fulu. Ncabwino ndigoneko pang'ono chabe." Pamenepo, Kalulu anagona tulo twakufa nato.

5

Fulu anafika pomwe Kalulu anagona. Iye anautsa Kalulu namuudza kuti apitilidze mpikisano othamanga koma kalulu anauza Fulu kuti, "pita, ndizakupeza kutsogolo."
Fulu anapitiliza ulendo wake pang'ono pang'ono. Patapita nthawi, Kalulu anauka

6

ndipo anaona Fulu pamtunda ali kupita.
Kalulu anayambanso kuthamanga kuti akapeze Fulu. Fulu ataona kuti Kalulu wauka ndipo ayamba kuthamanga, nayenso anaonjezera liwiro lake.

7

Mpikisano unakula pomwe Kalulu ndi Fulu anali pafupi kufika pa nthambo yotsirizira kuthamanga. Abuluzi awiri ndiwo anagwililira nthambo. Kalulu anayetsetsa kuthamanga mwamphamvu koma anali atacedwa kale ndipo Fulu anapambana mpikitsano.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nthano ya Kalulu ndi fulu
Author - Alifeyo Mkandawire and Impact Network
Illustration -
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs