

Kale-kale kunali banja la abambo Abvutika imene inkakhala pamudzi ochedwa Kapelepeta mdela la Mfumu Kathumba m'dziko la Zambia.
Banja imeneyi, inali ndi ana atatu, akazi awiri ndi mwamuna umodzi. Iwo anali kukhala bwino kotero kuti anthu
ena anali kukhumbira makhalidwe abanja limeneli.
Cifukwa ca makhalidwe ao abwino, Mulungu amawadatsa ndi zinthu zambiri. Iwo amakhala ndi zokolola zambiri. Banja limeneli limabzyala mbeu zosiyana-siyana monga cimanga, nshawa, mpenya dzuwa ndi
zina zotero.
Caka cina mdera la Mfumu Kathumba, mvula siinagwe mofikapo bwino. Tero munali njala yaikulu. Anthu anali kusowa komwe angathe ugula zakudya maka-maka ufa.
Cifukwa ca njala, anthu anali kugulitsa zinyama motsika mtengo.
Banja la abambo Abvutika linaganiza zoyamba malonda ogula ndi kugulitsa ufa. Anthu anapeza kogula ufa mofulumira ndiponso mosayenda mtunda wautali.
Caka cinatha ndipo bambo Abvutika anali ndi ndalama zambiri. Iwo anagula ngolo ndi ng'ombe makhumi atatu ndi zisanu. Anthu ambiri anacita kaduka cifukwa ca zinthu zimene bambo Abvutika anagula. Iwo anapatsidwa maina osiyana-siyana
M'caka ca 1990, abambo Abvutika anayamba kudwala matenda osaziwika bwino. Atapita kucipatala ca Nyanje, adotolo sanapeze matenda mthupi mwao. Abambo Abvutika anadwala kwambiri ndipo anawonda. Patapita matsiku, iwo anamwalira.
Amai Abvutika ndi ana ao atatu anaymba ukhala umoyo wamanzunzo cifukwa ca infa ya amuna ao.
Zakudya zinayamba kusowa cifukwa kulima kunali kovutikira. Amai Abvutika anali kukhala ndi cisoni pakuona momwe anali kuonekera ndipo naonso
anamwalira.
Ana abambo ndi mai Abvutika anayamba usautsidwa ndi anthu omwe anali kuwasunga. Anawalanda katundu onse ndipo anayamba kugona njala. Anawa anali kuwagoneka pa cikumba ca ng'ombe.
Coipa citsata mwine komanso Mulungu Sasiya ana ake. Mosapita nthawi, ng'ombe zomwe zinalandidwa ku Ana abambo Abvutika zinayamba kufa. Nayonso ngolo nakukhala zidutswa zidutswa.
Nkhani yamaphunziro pa ana amasiye awa inalipo. Mkulu mwaiwo dzina lake Malita anayamba sukulu pa Chinzule Primary School m'caka ca 1995. Mwacisoni, iye anali kulandidwa zobvala ndi kupandidwa popita kusukulu. Motero, iye analeka sukulu.
Patapita zaka, Malita anakwatilidwa mu boma la Sinda. Mwana wamuna dzina lake Ganizani anayamba kuwetera ng'ombe za amalume ake. Ngakhale kuti mwanayu anali kuwetera bwino ng'ombe, iye anali kunzunzidwa kwambiri akapita kunyumba.
Nthawi zambiri, iye anali kumanidwa cakudya. Ganizani amapita ndi njala kukaweta ng'ombe.
Tsiku lina, Ganizani anatsegulira ng'ombe napita nazo kuthengo ukazidyetsera ndi mnzace. Iwo anakumana ndi abambo ena kuthengo ali ndi nkhwangwa. Ganizani ndi mnzace anacita mantha ndipo anathawa. Ng'ombe zija zinalowa m'minda ndi kudya
cimanga.
Ganizani anapandiwa kwambiri cifukwa colekelera ng'ombe kudya cimanga m'minda ndipo anadwala. Pomwe anakhala bwino, Ganizani analeka kuwetera ng'ombe koma anaudzidwa kuti acoke panyumba.
Ganizani anapita ukakhala ndi mlongo wake
ndipo anayambitsidwa sukulu. Mwatsoka, mlongo wake nayenso anamwalira ndipo iye anabweleranso kumudzi. Ganizani anapitizabe sukulu. Iye anali kucita bwino kusukulu ndipo aziphunzitsi ake anali kum'konda kwambiri. Aziphunzitsi ambiri anali
kumpatsa ndalama zolipilira kusukulu ndi kugula zakudya. M'caka ca 2015, Ganizani anamalaza sukulu ndipo anayamba kugwira nchito ndi bungwe la Zambia Impact Network Ltd. Pali pano, Ganizani aphunzitsa anzake m'banja ija.
Ganizani athandizanso aja omwe anali kumnzunza.

