

Kale-kale, pamudzi wina wochedwa chenkhwe panali banja la anthu asanu ndi limodzi.
Abambo mulauzi ndiwo anali mutu wa banja ndipo akazi awo anali athandiwe
Anthu awa anali ndi ana awiri cabe. Odziwoka bwino ndi maina awo awa:
Poka anali mwana wa mwamuna ndipo Lozi anali mwana wa mkazi.
Banja ili inali ya anthu asanu ndi limodzi cifukwa anali kusunga agogo ake alozi onse amuna ndi akazi awo.
Tsiku lina agogo ake lozi akazi ndi amuna anali kuotha moto pa bwalo ndi azidzukulu awo awiri aja. Mwatsoka poka mlongo wake wa lozi sanakhale bwino pa mpando ndipo Lozi anamuonera.
Pokhala kuti Lozi anali wa cicepere, sanaugwire mtima.
Amvekere he-he-de! Naonako anthu inu!! Cotero onse anadabwa ndipo anapenya uku ndi uku kuti aone cimene Lozi anali kuseka mpaka anazindikira kuti ndi poka amene sanakhale bwino.
Cinali ca cisoni kwambiri kotero kuti poka anaganiza molakwika
nathawira kuthengo kwa yekha.
Iye anacoka pakhomo paja atanyamula nkhwangwa yake pa phewa nkulowera komwe anali kudziwa iye yekha.
Dzuwa linalowa ndipo aliyense anabwera pa khomo paja koma poka palibe. Anayembekezela kufika pakati pa usiku
koma poka sanaoneke ayi kunali cabe ziiiiii! Kutaca mmawa, abambo Mulauzi anakadziwitsa amfumu ndipo anapangana zoti amufune muthengo.
Azibambo onse a mmudzi anabalalikana mchire ndi mmapiri monse koma sanamupeze poka ayi.
Dzuwa linalowanso poka osaoneka pa khomo. Anayesa kupereka uthenga ku midzi ina yozungulira koma kunalibe amene anamupeza.
Patapita madiku atatu mbusa wa ng'ombe ali cikhalire kuchire, anaona kamsasa potero atafika pafupi, anaitana ndipo
Mau anamveka mkatimo anali a poka mnyamata wosowa uja.
Thawi yomweyo mbusa uja anathamanga kumudzi kukauza anthu. Amai ake anaphika nsima yoti abambo ake akamupase. Atafika kuja abambo ake anamuimbira kanyimbo kotere.
Odi poka, odi poka nyanjiwa×2 yai, yai nyanji ndiwe ndani ukuti odi pakhomo panga panjiwa?? Bambo ake, yai, yai nyanjiwa ndi wako naleta nsima dendeni nkhuku nyanjiwa.
Anapereka nsima ija koma poka anakana nati nifuna mlongo wanga Lozi
Ndiye adzanfipatse nsima. Ai ndithu munalobe mocotira koma kungopatsa Lozi nsima ija nanyamuka kukapereka ndithu.
Ha! Zacisoni atangofika pakhomo Lozi nayamba kuimba kanyimbo kaja, poka anatsegula citseko ali ndi nkhwangwa yake mmanja
kuti alandire nsima koma poka anayasamula nkhwangwa kuti ateme Lozi koma mwamwai inagweruka ikalibe kufika kwa Lozi. Anthu anali kuzungulira kamsasa kaja anabwera ndi kugwira dzanja poka ndi kudonsa apo lozi ali nje-nje-nje.
Kumufunsa cifukwa anacita zimenezi, poka anati ndinacita manyazi kwambiri poona mlongo wanga lozi akundiseka ndipo ndnakwiya kwabasi.
Ai ndithu akulu akulu anamutonthoza poka pa zomwe zinacitika. Nchembere za mmudzi zinakhazika pansi lozi kumuuza kuti sikwabwino kuseka ngati waona muthu wakhala koipa koma kudziwa momuuzira kapena kucokapo.

