

Kalele- kale munkhalango ina yochedwa chimutengo munali mkango omwe unali kukhala kumeneko, mukangoyu unali kunyadira mphamvu zake kotero kuti kunalibe nyama iliyonse imaopsa mkango.
Unali kupha nyama ina ilionse yomwe yapezeka, koma nyama
zina mwanyamazo zizinali kudyedwa ngati zaphedwa. Cifukwa ca cimeneci nyama zonse zinali kukhala zoopa kuti tizaziteteza bwanji umoyo wanthu ngati mkango wapiriza ndi nzelu zomwezi zakudya nyama munkhalango, anatero Kalulu.
"Mkango akupha nyama zambiri koma akudya cabe zochepa zina nyama zingo ziworera cabe" anadandaula kalulu.
Tifunika kupanga cinthu comwe cingati thandize kuti mkango ameneyu aleke kupha ndi kudya nyama mwacisawawa.
Tikamuleka tere tonse tizatha kufa anatero mnkhwere.
Ndipo nyama zonse zinakumana pamodzi, zinapangana kuti nyama zonse zipite kukakumana ndi Mkango.
Nyama zitafika kwa mkango zinati,
Odi- odi kuno amfumu. Ife tabwera kuno ndi pempho cabe anatero kalulu apo zitagwada zonse pansi. Kodi ingakhale pempho lanji? Unatero mkango mosangalala poona nyama zonse za munkhalango zagwada pansi.
Ndinu mfumu yamuno mu chire koma tsopano apa kuzakhala kulibe nyama zina zolamulira cifukwa tonse tizatha kufa kamba ka nzeru zanu mfumu. Anatero nyani kwa mkango. Ndipo kalulu anapitiriza kulankhula nati " tabwera kukuphemphani kuti
Muleke mkhalidwe wakupha nyama komansi tilonjeza kuti mmodzi mwa ife azayamba kubwera kwanu kukhala cakudya canu.anatero kalulu kudandaulira Mkango.
Ndipo kucokera pa tsiku limeneli nyama zonse zinali kungoganizira kuti kodi lero apite ndani kuti akhale cakudya ca mkango.
Tsiku lina nyama zonse zinasankha Kalulu kuti akaonane ndi mkango kuti akhale cakudya ca mkango kuti akhale cakudya
Ca mkango pa tsikulo. Koma kalulu kanali kanyams kocenjera kwambiri. Iye sanagune kuti akhale cakudya ca mkango. Kalulu anaona citsime cakale mumseu, citsimeco cinali cacitali kotero kuti nyama zonse zinali kuciopa.
Kalulu anaganiza njira
Zogonjetsera mkango. Kalulu snapita kukagona mphepete mwa citsime mpaka nthawi ya madzulo. Ndipo madzulo anapita kwa mkango. Pa nthawi imeneyo, mkango unali ndi njala kwambiri ndipo pamene unaona kalulu ali kubwera potero, mkango unakalipa
nati iwe kanthu kang'ono-ng'ono ubwera bwanji mochedwa tere? Nanga niciani ca citika ponitumizira kanyama kotere? Ine nizawapha onse anabangula mkango.
Kalulu anapereka mkango kucitsime kuti akamulatire mkango wina.
Atafika kalulu anamulatira citsime apo iye ali patali ndi citsimeco. Kalulu anati kwa mkango, thamangani mu citsime muzapezamo mikango ilikudya nyama zambiri zikulu-zikulu. Apo kalulu ali patali.
Mkango unasunzumira mucitsimeco ndipo unaona mkango wina osadziwa kuti ndi iye mwini cifukwa mucitsime munali madzi. Mkango unayamba kubangula apo cithunzi cake cicita cimodzi-modzi mmadzimo. Ndipo kupusa kwa mkango kunamuonetsa maloza apo
Kalulu wafa kuseka. Mkango unasunzumira mkati mwa citsime ndi ku jumphira momwemo ndipo unagwera mmadzi ndipo poona tero unakalipa kwambiri cifukwa sunapeze nyama ilionse koma madzi cabe.
Uko ndiko kunali kufa kwa mkango mkati mwa citsime. Kalulu anathamanga luwiro kupita kunali nyama zinzake kukapereka uthenga. Nyama zonse zinayamba kuyenda mosangalala cifukwa mkango uja unafa.

