

Panali nkhuku ndi mphemvu. Izi zacilengedwe zinapalana cibwenzi ndipo zinali kuyendelana kawiri - kawiri.
Tsiku lina nkhuku inayendera mphemvu kunyumba kwace. Mphemvu anakodwera kwambiri ndipo anakonzera nkhuku cakudya kuti idye. Nkhuku inakodwera kwambiri ndi kudya cakudya cija, itatha kudya cakudya inayamba kuceza.
Patapita Sabata imodzi mphemvu anaganiza kuti akayendere mzace nkhuku. Mphemvu inanyamuka ulendo opita kwa a nkhuku. Mphemvu itafika kwa a nkhuku, a nkhuku anakodwera kwambiri nalonjerana. Mosataya nthawi a nkhuku anakonza cakudya.
Atatha kudya a nkhuku ndi anzawo anayamba kuceza mnyumba, ndipo atatha kuceza Mphemvu anatsazika kuti apite kunyumba kwao. Nkhuku anakonza zinthu zakuti bwenzi lace linyamule monga izi: ufa, nshawa ndi zina zotero.
Awiriwa ananyamuka ulendo operekezana, ndipo mjira iwowa anali kukambilana nkhani zosiyana - siyana. Iwowa anayenda mtunda wautali cifukwa nkhuku inafuna kuthandiza mphemvu kunyamula zimene inapatsa mzace mphemvu.
Nkhuku ndi mphemvu zitayenda mtunda wautali, nkhuku inanva njala. Iyo ina ona - ona koma osaona cakudya cakuti ingadye. Motero inafuna kudya mphemvu.
Mphemvu atowona kuti nkhuku wamusinthira maganizo, iye anayamba kuthawa. Mphemvu tsopano inayamba kuuluka. Nkhuku nayo inayamba kuuluka. Koma cifukwa cakuti mphemvu ndi yaing'ono inauluka mofulumila kuthawa.
Mphemvu itawona kuti nkhuku ikubwelabe , iyo inauluka m'mwamba kwambiri. Ndipo mphemvu inathawira mnyumba ya munthu, m'mene inabisala, Nkhuku anayesetsa kufuna koma sanaionenso ai.
Kucokera apo mphemvu zinakhala cakudya ca nkhuku. Kotero kuti ngati nkhuku yaona mphemvu imadya kukhala ngati cakudya. kufikirana lero mphemvu zimakhala m'manyumba kubisala nkhuku kuti zingadyedwe.

