

Kale-kale, Mnkhwere ndi fulu anali pa ubwenzi wabwino kwambiri. Tsiku lina, fulu anali kuyenda-yenda mthengo kusakila zakudya.
Iye anakumana ndi mnkhwere bwenzi lake. "Bwanji mnzanga?" anatero mnkhwere. Uwoneka otopa kwambiri?
Kodi ciani comwe cabvuta? Anapilidza kufunsa mnkhwere.
Fulu anayankha natu, "njala yanipweteka kwambiri ndipo ndilibe zakudya zoti ndingadye. Ha! ha! ha! ha! anaseka mnkhwere mokweza kwambiri. Mnkhwere anati, ine ndili ndi zakudya zambiri.
Mnkhwere anauza fulu kuti, "ndili ndi zakudya zambiri. Nditsatire kuti ndikakugawireko. Fulu anatsatira bwenzi lake ndi cikhulupiliro cakuti zakudya wazipeza. Atafika kunyumba kwa mnkhwere, iwo anapeza amnkhwere ambiri ali kusangalala.
Ho! ho! ho!, ha! ha! ha! ha kusangalala kwakukulu.
Atafika, fulu anati, "mnzanga iwe, ndipatse zakudya ndibwerere kunyumba." Koma mnkhwere anadabwa monga sanadziwe kanthu nati, "zakudya! ngati ufuna zakudya, uyenera kukwera mtengoyu ndipo
utenge mowa onse ndi nthoci zomwe ziri m'mwambamo.
Atamva zimenezi, mtima wa fulu unapweteka kwambiri cifukwa anadziwa kuti sangathe ukwera mtengo. Mwacisoni, iye anabwerera ndi mkwiyo mumtima mwake. Iye anati mumtima, mnkhwere adzabweza
zowawa zomwe wandicita.
Fulu abwezera coipa.
Patapita zaka ziwiri, kunadza njala yaikulu padziko lapansi. Mnkhwere ankayenda-yenda m'mitengo kufuna-funa ndipo anakumana ndi bwenzi lake fulu.
"Kodi uli bwanji mnzanga?" anatero fulu.
Ukuoneka wacisoni kwambiri. Kodi ndi ciani comwe cakucitikira? anafunsa fulu. Mnkhwere anayankha nati, "mnzanga iwe, ndakhala ndili kusakila-sakila zakudya koma sindikuzipeza.
Zakudya! ha! ha! ha! ha! anaseka fulu mokweza mau ndipo anati,
ine ndili ndi zakudya ndipo ndikhodza kukugawilako ngati ufuna. Mnkhwere anati, conde! conde! ndipatsenkoni ndingafe ndi njala.
Fulu anati, coyamba uyenera kukatenga abale ako onse kuti muzalandire cakudya. "Cabwino." anatero mnkhwere.
Mnkhwere anayemda liwiro lokatenga abale ake.
Koma fulu mumtima anati, "sabola wakale sawawa, anandinyazitsa pamaso pa abale ake onse, inenso ndicita cimodzi-modzi pamaso pa abale anga."
Mnkhwere anabwera ndi abale ake onse ndipo fulu
anati, "ngati mufuna cakudya, muyenera kukasamba m'manja kumtsinje uja." Amnkhwere pakumva tero, anathamanga kukasamba m'manja kumtsinje. Koma amati akacoka kumtsinje kupita kukatenga zakudya, m'manja mwao munali kudanso cifukwa anali
anali kupondanso pansi.
Mnkhwere abwerera kunyumba.
Amnkhwere anapitiliza kusamba m'manja koma munali kuda ndithu cifukwa anali kuponda pansi poyenda.
Fulu pamodzi ndi banja lake, anaseka mokweza nati, ha! ha! ha! ho! ho! ho! ki! ki! ki!
Pomwepo mnkhwere anakumbukira zomwe anacita kwa bwenzi lake fulu ndipo anati mumtima, "fulu wabwezera." Mnkhwere pamodzi ndi banja lake anabwerera kwao momvetsa cisoni.

