Ine ndine insa. Ndine waliwiro kwambiri.
Ine ndine nyani. Nikonda kukwela-kwela mtengo ndi kudya nthochi.
Ine ndine fisi. Ndine wankhuli kwambiri.
Ine ndine mbizi. Ndine wokongola kwambiri kamba kautoto wanga.
Ine ndine fulu. Ndine nyama yoyenda ndi nyumba ndipo niyenda pang'ono-pang'ono kwambiri.
Ine ndine ng'ona. Ndine nyama ya m'madzi ndipo yoopeka.
Ine ndine mkango kapena kuti nkhalamu. Ndine mfumu ya mkhalango.
Ine ndine njobvu. Ndine wamphamvu kwambiri.
Ine ndine mvuu. Ndine nyama ya m'madzi.
Ine ndine nkhandwe. Ndipo nioneka ngati galu.
Ine ndine njati. Nioneka monga ng'ombe.
Ine ndine kalulu. Ndine wocenjera kwambiri.