

Bambo Malaiti ndi munthu wokalamba amene anakulila kumudzi ndipo angathe kutiuza zambiri za umoyo wakumudzi.
Kale-kale kumudzi kunalibe nyumba zamalata. Nyumba zinali za udzu komanso za laundi.
Azimai anali ndi nchito zambiri monga kusinja mphale. Kutubula ufa ndi zina zotele. Izi zinali nchito zowawa.
Izi zinali nchito za azimai kupepeta ndi kuuluza cimanga. Onani amai ali kuuluza cimanga.
Kale-kale timamwa madzi a dothi chifukwa timamwa madzi akumtsinje komanso amanyamulila mzipanda.
Azimai anali ndi mabvuto ambiri monga kunyamula nkhuni pa mutu. Izi zinali kucitika chifukwa kale-kale kunalibe ngolo ndi ngo'mbe zothandiza kunyamula nkhuni.
Abale anga kale-kale nchito zinali zowawa mbali zonse kwa azimai ndi azibambo chifukwa azi bambo anali kutema mtengo ikulu-ikuli.
Kale-kale nchito ya mdimba inali yowawa kwambiri chifukwa nthawi yothilira mbeu tinali kugwiritsa nchito kheni cabe.
Nthawi zonse amatsogola kumunda ndi azibambo apo ndi kuti azimai akugwira nchito zina monga kutapa madzi.
Atate ndi amai anali kulima. Iyi ndi nchito yomwe imafunika kugwirila pa modzi chifukwa imafuna mugwirizano kuti ipite pa tsogolo.
Madzulo akulu-akulu amaceza ndi adzukulu ndi kumaimba nzano apo akuotha moto.
Masiku ena sitinali kuimba nzano. Tinali kumvera wailesi.
Abale anga kale-kale kunalinso umphawi kwambiri kotelo kuti ana acimuna anali kuyenda alibe mala nthawi zambiri.
Kale-kale ana amalangizidwa mwa nkhanza chifukwa anali kuti akalakwa anali kumenyedwa kwambiri ndi makolo awo ndi mshapu.
Abambo anali kuvina atalezera ndi mowa wa cale. Uyu ndi mowa umene amaphikidwa ngati tatuta cimanga kuminda. Mowa umenewu umapsya paka pita masiku 7.

