

Mbizi analibe amai ndi atate ake. Analibe mbale wake kapena mlongo wake wakuti angaceze naye. Anali mbizi wayekha. Tsiku lina, anapita kuthengo.
Anali kukhala ndi maganizo chifukwa analibe omusangalatsa.
Tsiku lina anaganiza zopita kuthengo kukafuna bwenzi lake. Ali mthengomo nyani anabwera ali kulendewera mitengo. Nyani emweyo anaima ataona kuti mbizi ikumpenyetsetsa. "Khala bwenzi langa", mbizi inakuwa mokweza mau kulankhuza nyani.
Koma nyani atanva zimenezi anaopa ndikuthawa.
Nyani atathawa, mbizi anatsala yekha. Mbizi anadzadza ndi maganizo chifukwa anaganiza kuti wapeza bwenzi wake kukhala nyani, koma nyani anathawanso.
Iye anapitiliza ulendo wofuna-funa bwenzi.
Ali kupitiliza ndi ulendo wake, mbalame ya mtundu wakuda inabwera ikuuluka. Inaima ndikukhala pa msampo wa mtengo ndikupenya pansi panali mbiz. "Khala bwenzj langa", mbizi inakuwa, kukuwira mbalame.
Mbalame inaopa pomva mau a mbizi ndipo sinakonde kukhala bwenzi wa mbizi. Mofulumira, mbizi inakalipa ndipo inaganiza zopita ku mtsinje mokwinyirira.
Ulendo wopita ku mtsinje tsopano chifukwa anali atalema ndikunva ludzu litafikapo. Koma ngakhale anali kuyenda anali ndi maganizo oculuka.
"Nditani kuti ndipeze bwenzi la pa mtima?"
Iye anadzipenyesetsa pa thupi lake chifukwa sanali kumvetsetsa chifukwa comwe onse anali kuthawira akalankhula nawo.
Atatha kumwa madzi, anaimirira m'madzi momwemo kuganizira zabwenzi lake.
Mbizi inatuluka m'madzi ndikupitiliza ulendo wofuna bwenzi lake la pamtima. Ulendo unakula kwa iye mbizi chifukwa amayenda ndi maganizo oculuka kwambiri.
Ulendo wa mbizi kufuna bwenzi la pamtima.
Atayenda msenga wautali kwambiri, anaima nadzifunsa nati "kodi ndizapeza bwenzi langa lokondeka?"
Atazifunsa funso limeneli anamva mau onena kuti "sungamupeze bwenzi wako." Atacunguluka anaona nyamalikiti kuseli kwa mtengo.
Nyamalikiti anafendera kufupi ndi mbizi. Nyamalikiti inati, "sungapeze bwenzj ngati ukuwa motero," ungapeze bwenzi pokhapo utakhala bwenzi. Mbizi sanamvetse zomwe nyamalikiti ankhanena.
Mbizi inaona pansi potero, anaona fulu akubvutika kuti akwere pamwamba pa cimtengo comwe cinali cogona kuti apite ku mbali ina. Mbizi anapita ndikuthandiza fulu kumpereka ku mbali ina. "Zikomo" anatero fulu. Kodi dzina lako ndiwe ndani?
Mbizi mosagalala anati ndine mbizi. Pamenepo anazindikira comwe nyamalikiti amatanthauza. Wapeza bwenzi pambuyo pokhala bwenzi ndikuthandiza fulu.
Pomwepo ubwenzi wapondapo nane pondepo unayamba.

