

Onani mkango uyu. Mkango ndi nyama yoopysa mthengo. Nyama zonse zima thawa zikaona mkango cifukwa mkango umadya nyama zinzake. Tiyenera kuopa mkango.
Anthu ambiri amabwera kucokera kumaiko osiyana-siyana kuzaona nyama imeneyi. Ndipo ndi caphindu kusamalira nyama iyi cifukwa ithandiza dziko mnjira zosiyana-siyana. Dziko lathu lipanda kupeza ndalama cifukwa ca nyama yomeyi.
Tiyeni tisamalire nyama za mthengo.
Njobvu ndi nyama yaikulu mthengo. Njobvu ndi nyama yaphindu mdziko lathu la Zambia. Anthu ambiri amabwera kucoka kumaiko osiyana-siyana kuzaona njobvu. Ndipo iwo akabwera, abweretsa ndalama kuti cabe aone nyama.
Njobvu amasewenzetsa nchito zosiyana-siyana, ena amatengako minyanga zace pena ndiyo ndi zinchito zina zosiyana-siyana.
Nyama imadziwika kuti ili ndi mulomo wautali ndiponso ndi ya mphamvu kwambiri.
Akapokola pena kuti asilikali amene ateteza nyamazi aliko ndipo aliyense apezeka kupha nyamazi amagwiriwa ndi kumuika mndende. Tiyeni tisamalire nyama chifukwa zili zaphindu kwambiri.
Onana mbizi iyi ili imilire. Mbizi ndi nyama yamaonekedwe yabwino. Anthu ambiri amabwera kuona nyama iyi ndipo amabweretsa ndalama mudziko lathu.
Insa ndi nyama yocenjera mthengo. Timagwiritsa nchito nyama iyi mosiyana-siyana. Anthu ambiri amabwera kucokera kumaiko osiyana-siyana kuzaona nyama iyi. Imathandiza dziko lathu kuti lipite patsogolo chifukwa anthu amabweretsa ndalama.
Baka ndi nyoni ndi nyama zimene zipezeka pa nyumba. Baka ali ndi zinchito pena kuti phindu kwaise anthu. Timadya nyama ya baka, mazira yake ndiponso pena tingagulitse kuti tipeze ndalama.
Galu ndi nyama yofunikira pa nyumba pa anthu. Galu amatithandiza mnjira zosiyana-siyana. Monga kuteteza ife ngati kwabwera kawalala, kugwira nyama mthengo ndi zina zambira. Tiyeni tisamalire agalu.
Ngo'ombe ndi nyama yabwino kwambiri. Timagwiritsa nchito ngo'mbe mnjira zambiri. Timalimira, pena timadya nyama yake ndi kutengako mkaka.
Ngo'mbe ndi nyama zofunika pa umoyo wathu. Tiyeni tisamalire nyama izi.
Ngo'mbe ndi nyama imene anthu asunga pama nyumba awo ndi kugulitsa kuti apeze ndalama.
Abambo Chaiza asunga nkhuku pa nyumba pao. Nkhuku ndi zofunikira paumoyo wa munthu. Nkhuku zimathandiza anthu mnjira zambiri. Timapha nkhukj kuti tidye. Tingathe kugulitsa kuti tipeze ndalama. Nkhuku imaikira mazira omwe titha kugulitsa.
Cona ndi nyama imene ikhala mnyumba ya anthu. Anthu ambiri akonda kusunga cona pa nyumba pao chifukwa ca zocitika zina. Ena asunga cona kuti awagwirile akhoswe mnyumba mwao, enanso asunga cona chifukwa amawanvetsa bwino.
Cona ndi mdani wa akhoswe. Iye amagwira khoswe m'nyumba. Iye ali ndi maso amene aona bwino ngati kuli mdima.
Anthu ambiri akonda cona chifukwa ca zocita zace. Tiyeni tisamalire nyama iyi chifukwa itithandiza kwambiri.
Nkhumba ndi nyama imene imadya zinthu zauve kwambiri. Imadya zakudya zambiri ndiye chifukwa imaina. Anthu ambiri akonda kudya nyama yake ena ai. Nkhumba imagwiritsa nchito mnjira zosiyana-siyana. Anthu amasunga kuti azigulitsa.
Pena amapha ndi pangila ma soseji. Anthu ambiri akonda kudya nkhumba chifukwa ndi nyama ya mafuta kwambiri ndiponso nyama yake ndi yabwino kwambiri. Tiyeni tisunge bwino nkhumba zathu kuti tikhale ndi ndakama pena kuti nyama yabwino.

