

Tsiku lina a bambo Lufeyo anali kuyenda mthengo.Anali wokhumudwa cifukwa analibe nchito ndi ndalama yogulila zakudya.
Anaganiza zo puma pa chimtengo cakugwa cha kale. "Yaba"! anakuwa bambo Lufeyo pamene anagona pa chimtengo chakugwa co.
"Hmmmm", anaganiza, "chimtengo ici cioneka monga gome ndi mpando." Pomwepo bambo Lufeyo anaganiza nzeru zabwino. Ndinga sewenzetse chimtengo ici kupanga mpando ndi gome.
Bambo Lufeyo anatenga chimtengoco napita naco kunyumba.Anasewenzetsa mpeni wojuwila mathabwa napanga mathabwa kucokera ku chimtengoco.
Anasewenzetsa sando ndi misomali kupanga mpando ndi gome.Ananyamula mpando ndi gome napita nawo kutauni,pomwe anali kupita anakumana ndi mzimai wina yemwe anakonda mpando ndi gome lija.
Mzimai yo anagula mpando ndi gome kwa bambo Lufeyo,ndipo anapeza ndalama yokwanila kugula zakudya kunyumba ndi kugula zobvala za kusukulu za ana awo.
Tsiku losatila,bambo Lufeyo anapitanso kuthengo na tenga mitengo yambiri yopangila ,anapitirizabe kupanga mipando ndi magome ambili kuti adzigulitsa,ndipo malonda yawo yanali kuyenda bwino.
Malonda a bambo Lufeyo anapitabe patsogolo ndipo analembanso anthu ena owathandiza kupanga magome ndi mipando. Tsopano bambo Lufeyo malonda awo ndi aakulu opanga mipando magome ndipo apanga ndalama zambiri-mbiri.
Mwakupita kwa nthawi ,bambo Lufeyo anaganiza kuti ayambe kubyala mitengo ya paini yomwe siyacedwa kukula,kuti aziceka mathabwa yo pangila mipando ndi magome.Anachita zomwe anaganiza bambo Lufeyo ndipo anayamba kubyala mitengo.
Anaganiza zoyamba kubyala mitengo chifukwa ca kuti anaona kuti nchito inali kufuna kudula mitengo mchile popanda ubwezelapo komwe kuli ngati kuononga zacilengedwe.
Chifukwa ca maganizo abwino a bambo Lufeyo yobyala mitengo,ma bungwe ambiri yanacita cidwi ndi luso ya bambo Lufeyo ndipo anapasidwa udindo wophunzitsa anzao ndi kuwalimbikisa ubwino wobyala mitengo.

