Dorika wasenza mtsuko pamutu. Iye wabvala malaya ndi nsapato zofiira.
Yohane wakhala pam'pando. Iye ali kuphika nsima.
Mnyamata ali kudula nkhuni. Iye akugwiritsa ntchito nkhwangwa.
Yohane ali kudya nsima. Ali kudya nsima ya nyama.
Rakele ali kupita kusukulu. Wabvala yonifomu yokongola.
Atate ali kupsyera pakhomo. Ali kupsyera ndi cipsyelero.
Amai ali kucapa zobvala. Ali kucapa zobvala zao sopo.
Mnyamata ndi mtsikana ali kumenyana. kumenyana sikwabwino ai.
Maliya ali kuwerenga. Ali kuwerenga buku la nthano.
Tisiyenji ali kusinja. Ali kusinja mapira.
Mtsikana ali kusewera. Ali kusewera ndi mpira.