

"Bwanji?" Kalulu anapasta moni Fulu. Fulu anayakha nati, "Bwino."
Kalulu anauza Fulu kuti acite mpikisano othamanga. Fulu anamvomera.
Ndipo anapangana momwe mpikisano wao udzakha lira.
Anauza cule kuti akhale oyanganira ndipo bulu ogwira nthambo kotsilizira mpikisano.
M'mamawa kutaca, Kalulu ndi Fulu anauza cule oyanganira mpikisano wao othamanga kuti ayambitse.
Cule anawauza kuti akhale pamzele nayamba mpikisano othamanga.
Cule anaimikiza ndembela yofira kusonyeza kuyamba kwa mpikisano othamanga.
Kalulu podziwa kuti Fulu wakhalira kumbuyo kwambiri, anaganiza zopumula pamtengo nagona tulo. Fulu anafika panali kalulu napeza kuti iye wagona.
Fulu anadutsa mwacisisi nathamanga mofulumira kwabasi.
Pomwe kalulu anauka, anaona mapazi ya fulu mu njira. Ndipo iye anadziwa kuti fulu wadusa.
Motero kalulu anathamanga, nathamanganso kwambiri, koma sanamu - peze fulu ai.
Kalulu anathamanga naona fulu wafika Kale pomwe panali bulu ndi nthambo kumanja.
Fulu anadutsa nthambo ndikupabana mpikisano othamanga.
Kalulu analuza mpikisano othamanga.

